24 Ndikufuna kukuuzaninso kuti si zololeka kulandira msonkho kuchokera kwa ansembe, Alevi, oimba,+ alonda apakhomo, atumiki a pakachisi+ ndi anthu ogwira ntchito panyumba ya Mulungu. Musawakhometse msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu+ komanso msonkho wamsewu.