-
Deuteronomo 33:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
“Dziko lake lidalitsidwe ndi Yehova.+
Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba,
Ndi mame komanso madzi ochokera mu akasupe a pansi pa nthaka.+
14 Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,
Ndi zokolola zabwino kwambiri mwezi uliwonse,+
15 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa zamʼmapiri akale,*+
Ndi zinthu zabwino kwambiri zamʼmapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.
-
Yoswa 17:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Poyankha, Yoswa anauza anthu a fuko la Yosefe, omwe ndi ana a Efuraimu ndi Manase, kuti: “Ndinu ambiri ndipo ndinu amphamvu kwambiri. Simuyenera kukhala ndi gawo limodzi lokha,+ 18 koma mutengenso dera lamapiri.+ Ngakhale kuti ndi lankhalango, mudzagwetsamo mitengo ndipo gawo lanu likathera kumeneko. Mudzathamangitsa Akanani ngakhale kuti ndi amphamvu ndipo ali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.”+
-
-
-