-
Deuteronomo 23:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mbadwa ya Amoni kapena Mowabu isamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zawo zisadzalowe mumpingo wa Yehova mpaka kalekale, 4 chifukwa chakuti sanakuthandizeni pokupatsani chakudya ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ komanso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+
-