-
Oweruza 7:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Gidiyoni anatumiza uthenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu, wakuti: “Pitani ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna mʼmalo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ingʼonoingʼono mpaka ku Beti-bara. 25 Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi. Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitiriza kuthamangitsa Amidiyani+ ndipo anabweretsa mutu wa Orebi ndi wa Zeebi kwa Gidiyoni mʼchigawo cha Yorodano.
-