21 Sauli anayankha kuti: “Kodi ine si wa fuko la Benjamini, lomwe ndi lalingʼono kwambiri pa mafuko onse a Isiraeli?+ Ndipo kodi banja lathu si lalingʼono kwambiri pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Ndiye nʼchifukwa chiyani mukundilankhula chonchi?”