9 Kenako Doegi+ wa ku Edomu, mkulu wa atumiki a Sauli anayankha kuti:+ “Ineyo ndinaona mwana wa Jese atabwera ku Nobu kwa Ahimeleki, mwana wa Ahitubu.+
Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi wa ku Edomu, anapita kwa Sauli nʼkukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+