Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mbiri 17:16-22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako Mfumu Davide anakhala pansi pamaso pa Yehova ndipo anati: “Ndine ndani ine, inu Yehova Mulungu? Ndipo banja lathu* nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano?+ 17 Inu Mulungu, kuwonjezeranso pamenepa mwandiuza kuti nyumba ya ine mtumiki wanu idzakhazikika mpaka mʼtsogolo kwambiri+ ndipo inu Yehova Mulungu, mwanditenga ine ngati munthu woyenera kukwezedwa.* 18 Ndiyeno ine Davide mtumiki wanu ndinganene chiyani kwa inu poona ulemu umene mwandipatsa chonsecho inu mumandidziwa bwino ine mtumiki wanu?+ 19 Inu Yehova, chifukwa cha ine mtumiki wanu, komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,* mwachita zazikulu zonsezi pondidziwitsa kuti mumachita zazikulu.+ 20 Inu Yehova, palibe amene angafanane ndi inu+ komanso palibe Mulungu wina koma inu nokha.+ Zonse zimene tamva zikutsimikizira zimenezi. 21 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli?+ Inu Mulungu woona munapita kukawombola anthu anu.+ Komanso munadzipangira dzina pamene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha,+ pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu anu+ amene munawawombola ku Iguputo. 22 Munachititsa Aisiraeli kuti akhale anthu anu nthawi zonse.+ Ndipo inu Yehova munakhala Mulungu wawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena