14 Kenako Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli anati: “Malangizo a Husai mbadwa ya Areki ndi abwino+ kusiyana ndi a Ahitofeli.”+ Yehova anaonetsetsa kuti anthuwo asatsatire malangizo a Ahitofeli ngakhale kuti anali abwino. Yehova anachita zimenezi kuti abweretsere Abisalomu tsoka.+