-
2 Mbiri 9:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Makapu onse a Mfumu Solomo anali agolide, ndipo ziwiya zonse zamʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha. Panalibe chiwiya chasiliva chifukwa siliva sankaoneka ngati kanthu mʼmasiku a Solomo.+ 21 Zinali choncho chifukwa zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombozo zinkabweretsa golide, siliva, minyanga ya njovu,+ anyani ndi mbalame zotchedwa pikoko.
-