-
2 Mbiri 9:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Choncho Mfumu Solomo anali wolemera kwambiri ndiponso wanzeru kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi.+ 23 Mafumu onse apadziko lapansi ankafuna kuonana ndi Solomo kuti amve nzeru zake zimene Mulungu woona anaika mumtima mwake.+ 24 Anthuwo ankabweretsa mphatso monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide, zovala,+ zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi komanso nyulu* ndipo zimenezi zinkachitika chaka chilichonse.
-