-
Levitiko 9:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Pamapeto pake Mose ndi Aroni analowa mʼchihema chokumanako, kenako anatulukamo nʼkudalitsa anthuwo.+
Atatero ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse,+ 24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ nʼkunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi anayamba kufuula mokondwera ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
-