-
Danieli 5:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Mʼmalomwake mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo munalamula anthu kuti akubweretsereni ziwiya zamʼnyumba yake.+ Ndiyeno inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena mwamwera vinyo mʼziwiya zimenezi ndipo mwatamanda milungu yasiliva, yagolide, yakopa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala imene siona, kumva kapena kudziwa chilichonse.+ Koma Mulungu amene amakupatsani mpweya komanso amene ali ndi mphamvu zolamulira moyo wanu, simunamulemekeze.+
-
-
Habakuku 2:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kodi chifaniziro chosema chili ndi phindu lanji,
Pamene munthu wachisema?
Nanga chifaniziro chachitsulo ndi mphunzitsi wonama zili ndi phindu lanji,
Ngakhale kuti wochipanga amachikhulupirira,
Nʼkumapanga milungu yopanda pake yosalankhula?+
19 Tsoka kwa munthu amene amauza chikuni kuti: “Dzuka!”
Kapena mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”!
-