14 Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+