-
Deuteronomo 29:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’ 25 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti anaphwanya pangano la Yehova,+ Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene ankawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+
-
-
2 Mafumu 17:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anachita ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso zimene iye anawapatsa powachenjeza.+ Mʼmalomwake ankatsatira mafano opanda pake+ ndipo nawonso anakhala opanda pake.+ Ankatengera mitundu yowazungulira imene Yehova anawalamula kuti asamaitsanzire.+
-