-
2 Mafumu 9:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Zitatero Yehu anakoka uta wake nʼkubaya Yehoramu kumsana pakati pamapewa mpaka muviwo unatulukira pamtima pake ndipo Yehoramu anagwa mʼgaleta lake lankhondo.
-
-
2 Mafumu 10:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Kenako Yehu anawalemberanso kalata ina yonena kuti: “Ngati muli kumbali yanga ndipo muzimvera mawu anga, mudule mitu ya ana aamuna a mbuye wanu ndipo mawa nthawi ngati yomwe ino mubwere nayo ku Yezereeli kuno.”
Ana 70 a mfumuwo ankakhala ndi akuluakulu a mumzindawo omwe ankawasamalira. 7 Anthuwo atangolandira kalatayo, anatenga ana a mfumu 70 aja nʼkuwapha.+ Kenako anatenga mitu yawo nʼkuiika mʼmadengu ndipo anaitumiza kwa Yehu ku Yezereeli.
-
-
2 Mafumu 10:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, anauza asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta kuti: “Lowani muwaphe! Pasapezeke aliyense wothawira panja.”+ Choncho asilikali othamanga ndi othandiza pamagaletawo anayamba kupha anthuwo ndi lupanga nʼkumaponya mitembo yawo panja. Anakafika mpaka mʼchipinda chamkati* cha kachisi wa Baalayo.
-