Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 13:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Kenako Abisalomu analamula atumiki ake kuti: “Mukhale tcheru ndipo Aminoni akangofika posangalala ndi vinyo, ine ndikuuzani kuti, ‘Mupheni Aminoni!’ Zikatero mumuphe. Musaope. Ine ndi amene ndakulamulani. Muchite zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima.”

  • 2 Samueli 13:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Koma Abisalomu anathawa nʼkupita kwa Talimai,+ mwana wamwamuna wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Davide analira mwana wake kwa masiku ambiri.

  • 2 Samueli 15:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Abisalomu anatumiza akazitape ku mafuko onse a Isiraeli ndipo anawauza kuti: “Mukangomva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, mufuule kuti, ‘Tsopano Abisalomu ndi mfumu ku Heburoni!’”+

  • 2 Samueli 18:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma Yowabu anati: “Usandichedwetse iwe!” Atatero anatenga zobayira* zitatu ndipo anakabaya Abisalomu pamtima ali moyo pakati pa ziyangoyango za mtengo waukulu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena