-
Genesis 25:1-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura. 2 Patapita nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+
3 Yokesani anabereka Sheba ndi Dedani.
Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.
4 Ana a Midiyani anali Efa, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.
Onsewa anali ana aamuna a Ketura.
-