-
2 Mafumu 11:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndiyeno Yehoyada anachita pangano pakati pa Yehova, mfumu ndi anthu,+ kuti iwo apitiriza kukhala anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+ 18 Kenako anthu onse amʼdzikolo anapita kukachisi wa Baala nʼkukagwetsa maguwa ake ansembe,+ kuphwanyaphwanya mafano ake+ komanso anapha wansembe wa Baala+ dzina lake Mateni kutsogolo kwa maguwa ansembewo.
Ndiyeno wansembe Yehoyada anasankha anthu kuti aziyangʼanira nyumba ya Yehova.+
-