26“Upange chihema+ pogwiritsa ntchito nsalu 10 zopangira tenti. Nsaluzo zikhale za ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Pansaluzo upetepo+ akerubi.+
29 Pamakoma onse a nyumbayo a zipinda zonse ziwiri, zomwe ndi Malo Oyera Koposa komanso Malo Oyera, anajambulapo mochita kugoba akerubi,+ mitengo ya kanjedza+ ndi maluwa.+