-
2 Mafumu 12:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Yehoasi anauza ansembe kuti: “Mutenge ndalama zonse zimene anthu akubweretsa kunyumba ya Yehova za zopereka zopatulika,+ zomwe ndi ndalama za msonkho zimene munthu aliyense akupereka,+ ndalama zoperekedwa ndi anthu amene analonjeza ndiponso ndalama zonse zimene munthu aliyense watsimikiza mumtima mwake kuti abweretse kunyumba ya Yehova.+ 5 Wansembe aliyense azitenga ndalama zimenezi kwa anthu omwe apereka nʼkuzigwiritsa ntchito kukonza paliponse pamene nyumbayi yawonongeka.”*+
-
-
2 Mbiri 34:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Iwo anapita kwa Hilikiya mkulu wa ansembe nʼkumupatsa ndalama zimene anthu ankabweretsa kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi omwe anali alonda apakhomo, anatolera kwa anthu a fuko la Manase, la Efuraimu, kwa Aisiraeli onse,+ kwa Ayuda onse, anthu a fuko la Benjamini ndiponso kwa anthu onse okhala ku Yerusalemu. 10 Kenako ndalamazo anazipereka kwa anthu amene anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova. Ndiyeno anthu amene ankagwira ntchito panyumba ya Yehova anagwiritsa ntchito ndalamazo pokonza nyumbayo.
-