2 Ahaziya anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri.+
3 Ahaziya nayenso anayenda mʼnjira za anthu a mʼbanja la Ahabu+ chifukwa amayi ake ndi amene anali mlangizi wake kuti azichita zoipa.