-
2 Mafumu 12:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo ankapereka ndalama zimene awerengazo kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumba ya Yehova. Anthuwo ankagwiritsa ntchito ndalamazo polipira akalipentala, anthu omwe ankagwira ntchito yomanga panyumba ya Yehovayo,+ 12 amisiri omanga ndi miyala ndi anthu osema miyala. Ndalamazo anaguliranso matabwa ndi miyala yosema yokonzera nyumba ya Yehova ndiponso analipirira zonse zimene anagwiritsa ntchito pokonza nyumbayo.
-
-
2 Mbiri 34:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako ndalamazo anazipereka kwa anthu amene anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova. Ndiyeno anthu amene ankagwira ntchito panyumba ya Yehova anagwiritsa ntchito ndalamazo pokonza nyumbayo. 11 Anthu ogwira ntchitowa anapereka ndalamazo kwa amisiri ndi kwa omanga nyumba kuti agulire miyala yosema komanso matabwa olimbitsira nyumba ndiponso kuti akhome mitanda ya nyumba zimene mafumu a Yuda anazilekerera kuti ziwonongeke.+
-