-
Deuteronomo 29:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’ 25 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti anaphwanya pangano la Yehova,+ Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene ankawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+
-
-
1 Mbiri 28:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako ndipo uzimutumikira ndi mtima wonse+ komanso mosangalala, chifukwa Yehova amafufuza mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukamufunafuna, adzalola kuti umupeze,+ koma ukamusiya iye adzakusiya mpaka kalekale.+
-