-
1 Mbiri 28:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Anamupatsanso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyera kuzungulira kachisi, mosungira chuma cha nyumba ya Mulungu woona ndi mosungira zinthu zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+ 13 Komanso anamʼpatsa malangizo okhudza magulu a ansembe+ ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wapanyumba ya Yehova ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wapanyumba ya Yehova.
-
-
2 Mbiri 8:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Kuwonjezera pamenepo, Solomo anasankha magulu a ansembe+ kuti azitumikira mogwirizana ndi lamulo la Davide bambo ake. Anasankhanso Alevi kuti azikhala pamalo awo a ntchito nʼkumatamanda+ ndi kutumikira pamaso pa ansembe mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku. Komanso anasankha alonda apageti mʼmagulu awo kuti akhale mʼmageti osiyanasiyana+ chifukwa limeneli linali lamulo la Davide munthu wa Mulungu woona.
-