Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo atumiki ake atauzungulira.

  • 2 Mafumu 24:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha mʼnyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapanga kuti zikhale za mʼkachisi wa Yehova.+ Zimenezi zinachitika mogwirizana ndi zimene Yehova analosera.

  • 2 Mbiri 36:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Nebukadinezara anatenga ziwiya zina za mʼnyumba ya Yehova nʼkupita nazo ku Babulo ndipo anakaziika mʼnyumba yake yachifumu.+

  • 2 Mbiri 36:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+

  • Ezara 6:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ziwiya zagolide ndi zasiliva za mʼnyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara anatenga mʼkachisi yemwe anali ku Yerusalemu nʼkuzipititsa ku Babulo,+ zibwezedwe kuti zikaikidwe kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe mʼnyumba ya Mulungu.’+

  • Danieli 1:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+

  • Danieli 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo analamula kuti abweretse ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga mʼkachisi ku Yerusalemu.+ Anachita zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena amweremo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena