-
Ezara 5:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Komanso, mfumu Koresi inachotsa mʼkachisi wa ku Babulo ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara anazitenga mʼkachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, nʼkupita nazo kukachisi wa ku Babuloyo.+ Ndiyeno anazipereka kwa munthu wina dzina lake Sezibazara,*+ amene Koresi anamusankha kuti akhale bwanamkubwa.+
-
-
Hagai 1:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo, mʼmwezi wa 6, pa tsiku loyamba la mweziwo, mawu a Yehova anafika kwa Zerubabele+ yemwe anali bwanamkubwa wa Yuda mwana wa Salatiyeli, ndiponso kwa Yoswa yemwe anali mkulu wa ansembe mwana wa Yehozadaki. Mawuwa anafika kwa anthu amenewa kudzera mwa mneneri Hagai*+ kuti:
-