Levitiko 25:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Aisiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Choncho asamadzigulitse ngati mmene anthu amagulitsira kapolo. Deuteronomo 5:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakutulutsani kumeneko ndi dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula.+ Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muzisunga tsiku la Sabata. Deuteronomo 9:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Ine ndinayamba kupembedzera Yehova nʼkunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu. Anthuwa ndi anu,*+ amene munawawombola ndi mphamvu yanu ndipo munawatulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu.+ Deuteronomo 9:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Iwo ndi anthu anu komanso chuma chanu chapadera,*+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’”+
42 Aisiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Choncho asamadzigulitse ngati mmene anthu amagulitsira kapolo.
15 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakutulutsani kumeneko ndi dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula.+ Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muzisunga tsiku la Sabata.
26 Ine ndinayamba kupembedzera Yehova nʼkunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu. Anthuwa ndi anu,*+ amene munawawombola ndi mphamvu yanu ndipo munawatulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu.+
29 Iwo ndi anthu anu komanso chuma chanu chapadera,*+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’”+