9Aisiraeli onse analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo mʼBuku la Mafumu a Isiraeli. Ndipo Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.+
59 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+