64 Anthu onse analipo 42,360.+ 65 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200. 66 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu 245. 67 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.