-
Nehemiya 1:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Pa nthawiyo Haneni,+ mmodzi wa abale anga, anabwera limodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa mmene zinthu zinalili kwa Ayuda amene anathawa ku ukapolo+ komanso za Yerusalemu. 3 Iwo anandiyankha kuti: “Anthu amene anatsala mʼchigawo,* omwe anapulumuka ku ukapolo, ali pamavuto aakulu ndipo akunyozedwa.+ Nawonso mpanda wa Yerusalemu unagwa+ ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto.”+
-