-
Ezara 10:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Choncho lolani kuti akalonga athu aimire anthu onse+ ndipo aliyense mʼmizinda yathu, amene wakwatira mkazi wachilendo, abwere pa nthawi imene ikhazikitsidwe. Abwere limodzi ndi akulu a mzinda uliwonse ndi oweruza ake, mpaka titabweza mkwiyo wa Mulungu wathu amene watikwiyira kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.”
15 Koma Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yahazeya mwana wa Tikiva anatsutsa zimenezi, ndipo Mesulamu ndi Sabetai,+ omwe anali Alevi, anawathandiza.
-