-
Nehemiya 12:38, 39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Gulu lina loimba nyimbo zoyamika Mulungu linkayenda kumanzere, ndipo ine ndi hafu ya anthuwo tinkabwera pambuyo pawo. Oimbawo ankayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 39 Anadutsanso pamwamba pa Geti la Efuraimu,+ Geti la Mzinda Wakale,+ Geti la Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya ndi ku Geti la Nkhosa,+ ndipo anaima pa Geti la Alonda.
-