43 Atanena zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!”+ 44 Munthu amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro, nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Mʼmasuleni kuti athe kuyenda.”