-
Genesis 20:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Kenako Mulungu woona anamuuza mʼmalotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi, ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire. Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu. 7 Tsopano bweza mkaziyo kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri,+ ndipo adzakupempherera+ moti udzakhala ndi moyo. Koma ukapanda kumubweza, udziwe kuti iweyo ndi anthu ako onse ndithu mufa.”
-
-
Mateyu 27:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Komanso atakhala pampando woweruzira milandu, mkazi wake anamutumizira uthenga wakuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni chifukwa ine ndavutika kwambiri lero ndi maloto okhudza iyeyu.”
-