Miyambo 3:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa. Mateyu 11:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira zinthu zimenezi ndipo mwaziulula kwa ana aangʼono.+ Aroma 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa chifukwa analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo udakali wolumikizidwa kumtengowo chifukwa cha chikhulupiriro.+ Chotsa maganizo odzikuzawo, koma khala ndi mantha. Aroma 12:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera. Musamaganize modzikuza, koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musamadzione ngati anzeru.+ 1 Akorinto 1:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mukuona mmene anakuitanirani abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa, si ambiri amphamvu amene anaitanidwa, si ambiri a mʼmabanja olemekezeka.+
25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira zinthu zimenezi ndipo mwaziulula kwa ana aangʼono.+
20 Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa chifukwa analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo udakali wolumikizidwa kumtengowo chifukwa cha chikhulupiriro.+ Chotsa maganizo odzikuzawo, koma khala ndi mantha.
16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera. Musamaganize modzikuza, koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musamadzione ngati anzeru.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa, si ambiri amphamvu amene anaitanidwa, si ambiri a mʼmabanja olemekezeka.+