4 Yehova Mulungu wanu akadzawathamangitsa pamaso panu musadzanene mumtima mwanu kuti, ‘Yehova watilowetsa mʼdziko lino kuti tilitenge kukhala lathu, chifukwa chakuti ndife olungama.’+ Mʼmalomwake, Yehova akuthamangitsa mitundu iyi pamaso panu chifukwa choti ndi yoipa.+