2 Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.+
Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.
3 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.
Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.
4 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+
Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.
5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.
Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+