-
Yesaya 17:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Tamverani! Kuli chipwirikiti cha anthu ambirimbiri,
Amene akuchita mkokomo ngati nyanja.
Mitundu ya anthu ikuchita chipolowe,
Ndipo phokoso lawo lili ngati mkokomo wa madzi amphamvu.
13 Mitundu ya anthu idzachita phokoso ngati mkokomo wa madzi ambiri.
Iye adzawadzudzula ndipo iwo adzathawira kutali.
Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo mʼmapiri
Ndiponso ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo yamkuntho.
-
-
Yesaya 57:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde, imene singathe kukhala bata,
Ndipo madzi ake akuvundula zomera zamʼnyanjamo ndiponso matope.
-