14 Amameretsa msipu kuti ngʼombe zidye,
Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+
Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke mʼnthaka
15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,+
Mafuta amene amachititsa kuti nkhope ya munthu isalale,
Ndiponso chakudya chimene chimapereka mphamvu kwa munthu.+