-
Yoswa 3:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Onyamula Likasawo atangofika pamtsinje wa Yorodano, nʼkuponda madzi a mʼmphepete mwake (mtsinje wa Yorodano unkasefukira+ nyengo yonse yokolola), 16 madzi ochokera kumtunda anaima ngati khoma. Ndipo anakhala ngati damu lomwe linasefukira mpaka kukafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani. Koma madzi akumunsi omwe ankapita kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere,* anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anagawikana, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
-