11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa.+
Ndipo ngakhale mʼnyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ akutero Yehova.
12 “Choncho njira zawo zidzakhala zoterera komanso zamdima.+
Adzakankhidwa ndipo adzagwa.
Chifukwa ndidzawagwetsera tsoka
Mʼchaka chimene ndidzawalange,” akutero Yehova.