-
Deuteronomo 6:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 mwana wanuyo mudzamuyankhe kuti, ‘Tinali akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu.
-
-
Deuteronomo 11:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mawu angawa muwasunge mʼmitima yanu ndipo muziwatsatira pa moyo wanu. Muwamange padzanja lanu kuti muziwakumbukira ndipo akhale ngati chomanga pachipumi panu.*+ 19 Muziphunzitsa ana anu mawu amenewa, ndipo muzilankhula nawo mawuwa mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+
-
-
Yoswa 4:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Miyalayo idzakhala chizindikiro kwa inu. Ana anu* akamadzafunsa mʼtsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 7 Muzidzawauza kuti: ‘Nʼchifukwa chakuti madzi amumtsinje wa Yorodano anagawikana chifukwa cha likasa+ la pangano la Yehova. Likasalo likudutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinjewo anagawikana. Miyalayi ndi yoti izikumbutsa Aisiraeli zimenezo mpaka kalekale.’”+
-