17 Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata,+
Ndipo mpaka pano ndikupitiriza kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+
18 Ngakhale nditakalamba nʼkumera imvi, inu Mulungu musandisiye.+
Ndiloleni kuti ndiuze mʼbadwo wotsatira za mphamvu zanu
Komanso za nyonga zanu kwa onse obwera mʼtsogolo.+