16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa, ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+