-
Numeri 11:31-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Kenako Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri, ndipo inazimwaza kuzungulira msasawo+ mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali zonse za msasawo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinaunjikana mulu wokwana pafupifupi masentimita 90* kuchokera pansi. 32 Ndiyeno anthuwo anayamba kugwira zinzirizo. Anazigwira masana onse, usiku wonse, mpakanso tsiku lotsatira osapuma. Palibe amene anagwira zosakwana mahomeri* 10 ndipo ankaziyanika paliponse, moti zinangoti mbwee, pamsasa wonsewo. 33 Koma nyamayo idakali mʼkamwa mwawo, asanaitafune nʼkomwe, mkwiyo wa Yehova unayakira anthuwo. Ndipo Yehova anayamba kuwalanga moti anthu ambiri anaphedwa.+
34 Malo amenewo anawatchula kuti Kibiroti-hatava,*+ chifukwa anakwirirapo anthu amene anasonyeza mtima wadyera.+
-