-
Ekisodo 10:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Dzombelo linafika mʼdziko lonse la Iguputo nʼkufalikira mʼmadera onse adzikolo+ ndipo linawononga kwambiri.+ Dzombe lambiri ngati limeneli linali lisanagwepo nʼkale lonse ndipo silidzagwanso lambiri ngati limeneli. 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse yamʼdzikolo ndipo dziko linachita mdima. Dzombelo linadya zomera zonse zamʼdzikolo ndi zipatso zonse zamʼmitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala, moti sipanatsale chobiriwira chilichonse mʼmitengo kapena mʼminda mʼdziko lonse la Iguputo.
-