3 Kenako Samueli anauza Aisiraeli onse kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova ndi mtima wanu wonse,+ chotsani milungu yachilendo+ komanso zifaniziro za Asitoreti,+ ndipo muzitumikira Yehova yekha ndi mtima wanu wonse.+ Mukatero, adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisiti.”+