22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho.+ Ndidzakuuza malamulo onse oti ukauze Aisiraeli kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni.
4 Choncho anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ analinso komweko limodzi ndi likasa la pangano la Mulungu woona.