23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 24 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mʼmwezi wa 7, pa tsiku loyamba la mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, ndipo lipenga likalira+ muzisonkhana kuti mulambire Mulungu.