-
Ekisodo 20:2-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+ 3 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+
4 Musadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi.+ 5 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.
-